Kutumikila Mulungu Mchipani cha maPallottines
ngati Wansembe Kapena Mblazala

Atumiki a Mulungu mChipani cha maPallottines akupezeka mDziko lonse la pansi pano.
– Tsatani Ambuye Yesu. –
Lowani chipani cha maPallottines pamene akukhazikitsa utumiki wawo kuno ku Malawi.

Nkhoswe ya maPallottines

Amayi Maria Mfumukazi ya Apostoli ndiye nkhoswe ya mamembala onse a chipani cha maPallottines. Chipani cha maPallottines adayambitsa ndi Saint Vincent Pallotti amene anali wansembe wampingo wa katolika mdziko la Italy. Chipanichi dzinalake lomwe bambo Pallotti adachiptsa ndi Society of Catholic Apostolate, mwachidule! SAC,

Atumikiwa amatchedwa maPallottines potengela kuti chipanichi adayambitsa ndi bambo Vincent Pallotti a kuRoma.

Bambo Vincent Pallotti adatuma mmisili kuti ajambule chithunzi chokhala ndi Amayi Maria ndi amayi ena awiri pamodzi ndi apostoli a Ambuye Yesu, akulandila mphamvu za Mzimu Oyera pa tsiku la Pentecost, mchipinda chamwamba chotchedwa Senakolo.

Chithunzichi chimatanthauza kuti mpingowonse wa wokhulupilira Mulungu, ansembe komanso akhrisitu eniake adalandila mphatso za Mzimu Oyera kuti akhale atumiki authenga wabwino wakuuka kwa akufa kwa Ambuye Yesu. Ndiye kuti munthu wina aliyense, wamwamuna kapena wamkazi, mn’gono kapena wamkulu, wolemera kapena wosauka, aliwoyitanidwa kutsatira Ambuye Yesu Khristu.

Malumbilo a maPallottines

Atumikiwa alipo pafupifupi 2 500 ansembe komanso ablazala amene akutumikila Mulungu ndi anthu onse, modzicheptsa ndi mokhulupilika pokhala mchipani. Atumikiwa amalonjeza kukhala opanda banja, kukhala omvera, kukhala mosadziunjikila chuma, kukhala opilira, komanso kugawana ndianthu onse zimene Mulungu adatipatsa mwachifundo chake, ndipo kukhala ndimtima wotumikila mwachimwemwe.

Mary the Mother of God is the patron saint of the Pallottines

The original painting “Mary the Untier of Knots” is kept in Augsburg in Germany, not far from our provincialate. The painting is more than 300 years old and known and loved all over the world. Pope Francis himself commissioned a copy for the Vatican. We the Pallottines have had another special copy made for Malawi.

The Pallottines

“Mulungu ndichikondi! Aliyense amene amakonda mzake amakhala mwa Mulungu.” (1 Yohane 4:16)

MaPallottines ndi atumikia Mulungu mu Mpingo wapa malo ponse, Mpingo wa Katolica. MaPallottines alindicholinga chotsitsimutsa Chikhulupiliro ndikuyatsanso moto wa Chikondi padziko lapansi ndikupititsa patsogolo Chikhulupiliro ndi Chikondi cha Mulungu.

maPallottines ndiatumiki amene aliwokonzeka kutumikila muMpingo kupititsa patsogolo umodzi pakati pa mitundu yaanthu kuti maso mphenya a bamboo Vincent Pallotti wositha dziko lapansi afike pakepenipeni.

Atumikwa amagwira ntchito mosamvetsera kutopa popititsa patsogolo chilingamo mdi mtendere. Powerengera mphatso zosiyana siyana zimene Mulungu adatipatsa anthufe padziko lapansi pano ndiphamvu zimene mulungu adatipatsa kuti tigwiritse ntchito mumpingo ndi mdziko lino laMalawi kuti tonse pamodzi timange mpingo wa Ambuye.

maPallottines ali ndichikhulupiliro chozama kuti akhristu onse akhale ogwrizana pakumanga mpingo wa Mulungu. Ndizachidziwikilre kuti munthu aliyense akuyitanidwa mosiyana ndimzake, komabe pakugwira ntchito limodzi ndipamene tingamange mpingo wamphamvu wa Ambuye.

Vincent Pallotti

Bambo Vincent Pallotti adagwiritsitsa mau aja akuti Mulungu ndi Chikondi chopanda malire, kotero kuti adati, ndibwino kuti tiziliona dziko ndi maso a Mulungu ngakhale kuti nthawi zina m’dziko muli zowawa ndizokhumudwitsa nthawi-ndi-nthawi.

MaPallottines ndi anthu atcheru andi ogwirizana ndikulimbikitsana kuchitapo kanthu paqkukometsa moyo wa anthu padziko lapansi potsatila masomphenya a bamboo Vincent Pallotti. MaPallottines ndi atumiki okonzeka kuchitira umboni chikhulupiliro mwa Mulungu pamene dziko likupitapatsogolo m’njira zosiyanasiyana, pakupereka Uthenga wa Ambuye motsata maphunzitso a Mpingo opezeka mmaphunzitso a Msonkhano wa ku Vatikani wa Chiwiri (Vatican Council II) ndi malandizo a Apapa

Bambo Vincent Pallotti amaphunzitsa kuti, ubale wa Mulungu ndi anthu ake, ndiubale wodalilana, ndipo chikondi ndicho chimapatsa moyo ubalewu. Ndipo amene amakondana ndiamene amachitila umboni motsimikiza za ubale waMulungu ndi anthu ake.

Akhristu eniake akuyenera kutengapo mbali mogwirizana, pogwirtsa ntchito zaulere zimene Mulungu adawapatsa kuti pakhale umodzi pakati pa anthu ake a Mulungu. Kotero kuti mpingo ukhaledi chitsanzo cha Umodzi ndi Chipulumutso padziko lino lapansi.

Kukhala limodzi ndi maPallottines

Povomeleza kuitanidwa kwawo maPallottines, ali ndichikhulupiliro cholimba, ndipo akudzipereka kutumikila Mulungu ndi Mpingo wa ku Malawi.

Lowani mchipani cha maPallottines ndikutengako mbali pokhazikitsa chipani cha maPallottines kuno ku Malawi pakukhala wansembe kapena mblazala.

Tifunseni njira yolowera mchipani cha maPallottines

Tidzakuthandizani moyera ngati muli wokondweretsedwa kulowa mchipani mukatifunsa potiyimbila foni kapena kutilembela kalata.

Zina Zomwe zikusoweka kuti mulandilidwe

Ndondomeko ya ulendo wanu wamoyowanu pamaphunziro komanso utumikiwanu pakati pananzanu Curriculum Vitae / CV
Uyenera kukhala ndi ma Points kuyambira 25
Kalata yofotokoza zifukwa zimene mukufunila kulowa chipanichi momveka bwino.
Mukatero mudzaitanidwa kuti tionane maso ndimaso.
Mukatero tidzagwirizana ndondomeko yammene tingakuthandizireni kupititsa ndikupherezela kuitanidwa kwanu chipanichi.
Mukhale mkhristu wobatizidwa wa mpingo wa Katolika.
Mukhale ndizaka zosachepera 18
Mukhale mutamaliza kapena mukumaliza maphunziro a Sekondare, ndiponagti mwawonjezera ndi maphunziro a maluso ena kwaife ndinkhani yabwinonso.
Ndikoyera kukhala olankhulako chilankhulo cha chingerezi,
Mukhale ndimoyo mathanzi, komanso mmutu mukhale molongosoka, komanso oyesetsa kukhala bwino ndi anzanu.

Nthambi yoyamba kulowa mmoyo wa mchipani cha maPallottines: (Postulancy) ndi Novitiate

Iyi ndithawi yomwe amene akufuna kulowa mchipani ampatsidwa maphunziro oyamba pamene munthu akufuna kutumikila Mulungu mchipani. Ndipo amathandizidwa kuti azindikile ngati ali woneradi kutumikila Mulungu mmoyo wamchipani. Pakutha pa nyengo iyi kandideti ngati ali wonera amaloledwa kupitiliza maphunziro ku Novitiate, kenaka amatumizidwa kukachita maphunziro a Philosophy ndikumaliza ndi maphunziro a Theology.

Cholinga cha utumiki wathu ndikupititsa patsogolo moyo wamunthu wina aliyense pano padziko lapansi. Tiyeni mogwirizana titsitsimutse moyo wa Chikhulupiliro komanso Chikondi pakati pa munthu ndi mzake.

Ambuye Mulungu wachifundo ndi chikondi chopand malire atsogolere moyo wakuitanidwa kwanu.

We have a mission – to change the world!

We change ourselves and help to build the Kingdom of God which is among us here and now.

Vincent Pallotti is calling us to raise awareness among all the faithful that they have an apostolic vocation which they should nurture. It is our aim to unite and proclaim Jesus Christ’s message of salvation.

Help us to renew Christian faith and rekindle love. Help us to bring the Gospel to others.

We change ourselves and help to build the Kingdom of God which is among us here and now.

Vincent Pallotti is calling us to raise awareness among all the faithful that they have an apostolic vocation which they should nurture. It is our aim to unite and proclaim Jesus Christ’s message of salvation.

Help us to renew Christian faith and rekindle love. Help us to bring the Gospel to others.

Lembani kalata kwa

Bambo Rodrick White Phiri SAC
Pallottines
P.O.B. 406 Lilongwe
Malawi

Kapena online:
vocation@pallottinesmalawi.org

Das könnte Sie auch interessieren

Mitreden, Mitmachen, Mithelfen!

Erfahren Sie mehr über unsere Gemeinschaft:

Sich einbringen ins Ganze:

Unsere Köpfe und ihre Geschichten:

Berufung: Ein Weg für dich?

Gemeinsam die Welt verändern!

Print Friendly, PDF & Email